Yoswa 23:5-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Ndipo Yehova Mulungu wanu Iyeyu adzawapitikitsa pamaso panu, ndi kulanda dziko lao kuwacotsa pamaso panu, ndipo mudzalandira dziko lao likhale colowa canu; monga Yehova Mulungu wanu ananena ndi inu.

6. Koma mulimbike mtima kwambiri kusunga ndi kucita zonse zolembedwa m'buku la cilamulo ca Mose, osacipambukira kulamanja kapena kulamanzere;

7. osalowa pakati pa amitundu awa otsala mwa inu; kapena kuchula dzina la milungu yao; osalumbiritsa nalo, kapena kuitumikira, kapena kuigwadira;

8. koma muumirire Yehova Mulungu wanu, monga munacita mpaka lero lino.

9. Pakuti Yehova anaingitsa pamaso panu mitundu yaikuru ndi yamphamvu; koma inu, palibe munthu anaima pamaso panu mpaka lero lino.

10. Munthu mmodzi wa inu adzapitikitsa anthu cikwi cimodzi; pakuti Yehova Mulungu wanu ndiye amathirira inu nkhondo monga ananena ndi inu.

11. Potero mudzisamalire ndithu kuti mukonde Yehova Mulungu wanu.

Yoswa 23