3. Koma Tselofekadi, mwana wa Hefere, mwana wa Gileadi, mwana wa Makiri, mwana wa Manase, analibe ana amuna koma ana akazi ndiwo; ndipo maina a ana ace akazi ndiwo: Mala, ndi Nowa, Hogila, Milika ndi Tiriza.
4. Ndipo anayandikira pamaso pa Eleazare wansembe, ndi pamaso pa Yoswa mwana wa Nuni, ndi pamaso pa akalonga, ndi kuti, Yehova analamulira Mose atipatse colowa pakati pa abale athu; cifukwa cace anawapatsa monga mwa lamulo La Yehova, colowa pakati pa abale a atate wao.
5. Ndipo anamgwera Manase magawo khumi, osawerenga dziko la Gileadi ndi Basana lokhala tsidya lija la Yordano:
6. popeza ana akazi a Manase adalandira colowa pakati pa ana ace amuna; ndi dziko la Gileadi linakhala la ana a Manase otsala.