31. ndi Gileadi logawika pakati, ndi Asitarotu ndi Edrei, midzi ya ufumu wa Ogi m'Basana, inali ya ana a Makiri mwana wa Manase, ndiwo ana a Makiri ogawika pakati, monga mwa mabanja ao.
32. Izi ndi zolowazi Mose anazigawira m'zidikha za Moabu, tsidya ilo la Yordano ku Yeriko, kum'mawa.
33. Koma pfuko la Levi, Mose analibe kulipatsa colowa: Yehova Mulungu wa lsrayeli, ndiye colowa cao, monga ananena nao.