56. Iye wakudya thupi langa indi kumwa mwazi wanga 12 akhala mwa Ine ndi Ine mwa iye.
57. Monga Atate wamoyo anandituma Ine, ndipo Inenso ndiri ndi moyo cifukwa ca Atate; momwemo wondidya Ine, iyeyu adzakhala ndi moyo cifukwa ca Ine.
58. 13 Mkate wotsika Kumwamba ndi umenewu: si monga makolowo, anadya namwalira; iye wakudya mkate umene adzakhala ndi moyo nthawi zonse.
59. Izi ananena m'sunagoge, pakuphunzitsa m'Kapernao.
60. 14 Pamenepo ambiri a akuphunzira ace, pakumva izi, anati, Mau awa ndi osautsa; akhoza kumva awa ndani?
61. Koma Yesu podziwa mwa yekha kuti akuphunzira ace alikung'ung'udza cifukwa ca ici, anati kwa iwo, ici mukhumudwa naco?