45. Musayesa kuti Ine ndidzakunenezani inu kwa Atate; 6 pali wakukunenezani, ndiye Mose, amene inu mumtama.
46. Pakuti mukadakhulupirira Mose, mukadakhulupirira Ine; 7 pakuti iyeyu analembera za Ine.
47. Koma ngati simukhulupirira malembo a iyeyu, mudzakhulupirira bwanji mau anga?