Yohane 4:19-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

19. Mkazi ananena ndi iye, Ambuye, ndizindikira kuti muli Mneneri.

20. Makolo athu analambira m'phiri ili; ndipo inu munena, kuti m'Yerusalemu muli malo ozenera kulambiramo anthu.

21. Yesu ananena naye, Tamvera Ine, mkazi iwe, kuti ikudza nthawi, imene simudzalambira Atate kapena m'phiri ili, kapena m'Yerusalemu.

Yohane 4