11. Mkaziyo ananena ndi Iye, Ambuye, mulibe cotungira madzi, ndi citsime ciri cakuya; ndipo mwatenga kuti madzi amoyo?
12. kodi muli wamkuru ndi atate wathu Yakobo amene anatipatsa ife citsimeci, namwamo iye yekha, ndi ana ace, ndi zoweta zace?
13. Yesu anayankha nati kwa iye, Yense wakumwako madzi awa adzamvanso Iudzu;
14. koma iye wakumwa madzi amene Ine ndidzampatsa sadzamva ludzu nthawi zonse; koma madzi amene Ine ndidzampatsa adzakhala mwa iye kasupe wa madzi otumphukira ku moyo wosatha.
15. Mkaziyo ananena kwa iye, Ambuye, ndipatseni madzi amene, kuti ndisamve ludzu, kapena ndisadze kuno kudzatunga.
16. Yesu ananena kwa iye, Muka, kamuitane mwamuna wako, nudze kuno.
17. Mkazi anayankha nati kwa iye, Ndiribe mwamuna. Yesu ananena naye, Wanena bwino, kuti mwamuna ndiribe;
18. pakuti wakhala nao amuna asanu; ndipo iye amene ukhala nave tsopano sali mwamuna wako; ici wanena zoona.
19. Mkazi ananena ndi iye, Ambuye, ndizindikira kuti muli Mneneri.
20. Makolo athu analambira m'phiri ili; ndipo inu munena, kuti m'Yerusalemu muli malo ozenera kulambiramo anthu.
21. Yesu ananena naye, Tamvera Ine, mkazi iwe, kuti ikudza nthawi, imene simudzalambira Atate kapena m'phiri ili, kapena m'Yerusalemu.
22. Inu mulambira cimene simucidziwa; ife tilambira cimene ticidziwa; pakuti cipulumutso cicokera kwa Ayuda.
23. Koma ikudza nthawi, ndipo tsopano iripo, imene olambira oona adzalambira Atate mumzimu ndi m'coonadi; pakuti Atate afuna otere akhale olambira ace.
24. Mulungu ndiye mzimu; ndipo omlambira iye ayenera kumlambira mumzimu ndi m'coonadi.
25. Mkazi ananena ndi Iye, Ndidziwa kuti Mesiya adza (wochedwa Kristu): akadzadza Iyeyu, adzatiuza zonse.
26. Yesu ananena naye, Ine wakulankhula nawe ndine amene.
27. Ndipo pamenepo anadza ophunzira ace; nazizwa kuti analinkulankhula ndi mkazi; koma panalibe wina anati, Mufuna ciani? kapena, mulankhula naye ciani?
28. Pamenepo mkazi anasiya mtsuko wace, namuka kumudzi, nanena ndi anthu,
29. Tiyeni, mukaone munthu, amene anandiuza zinthu ziri zonse ndinazicita: ameneyu sali Kristu nanga?
30. Anaturuka iwo m'mudzi ndipo analinkudza kwa iye.
31. Pa mphindikati iyi ophunzira ace anampempha iye, ndi kunena, Rabi, idyani.