1. Cifukwa cace pamene Ambuye anadziwa kuti Afarisi adamva kuti Yesu anayesa anthu ophunzira, nawabatiza koposa Yohane
2. (angakhale Yesu sanabatiza yekha koma ophunzira ace),
3. anacokera ku Yudeya, namukanso ku Galileya.
4. Ndipo anayenerakupita pakati pa Samariya.