26. Pamenepo Yesu pakuona amace, ndi wophunzira amene anamkonda, alikuimirirako, ananena kwa amace, Mkazi, taonani, mwana wanu!
27. Pamene ananena kwa wophunzirayo, Taona, amai wako. Ndipo kuyambira ora lomweli wophunzirayo ananka naye kwao.
28. Citapita ici Yesu, podziwa kuti zonse zidatha pomwepokuti lembo likwaniridwe, ananena, Ndimva ludzu.
29. Kunaikidwako cotengera codzala ndi vinyo wosasa; cifukwa cace anazenenga cinkhupule codzaza ndi vinyo wosasayo pa phesi lahisope, nacifikitsa kukamwa kwace.
30. Pamene Yesu tsono adalandira vinyo wosasayo anati, Kwatha; ndipo anawerama mutu, napereka mzimu.