19. Koma Pilato analemba lembo, naliika pamtanda. Koma panalembedwa, YESU MNAZARAYO, MFUMU YA AYUDA.
20. Ndipo lembo ilo analiwerenga ambiri a Ayuda; cifukwa malo amene Yesu anapaeikidwapo anali pafupipa mudziwo; ndipo linalembedwa m'Cihebri, ndi m'Ciroma, ndi m'Cihelene.
21. Pamenepo ansembe akulu a Ayuda, ananena kwa Pilato, Musalembe, Mfumu ya Ayuda; koma kuti Iyeyu anati, Ndiri Mfumu ya Ayuda.
22. Pilato anayankha, Cimene ndalemba, ndalemba.