Yohane 17:1-5 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Zinthu izi analankhula Yesu; ndipo m'mene anakweza maso ace Kumwamba, anati, Atate, yafika nthawi; lemekezani Mwana wanu, kuti Mwana wanu akulemekezeoi Inu;

2. monga mwampatsa iye ulamuliro pa thupi liri lonse, kuti onse amene mwampatsa iye, awapatse iwo moyo wosatha.

3. Koma moyo wosatha ndi uwu, kuti akadziwe Inu Mulungu woona yekha, ndi Yesu Kristu amene munamtuma.

4. Ine ndalemekeza Inu pa dziko lapansi, m'mene ndinatsiriza nchito imene munandipatsa ndicite.

5. Ndipo tsopano, Atate Inu, lemekezani Ine ndi Inu nokha ndi ulemerero umene ndinali nao ndi Inu lisanakhale dziko lapansi.

Yohane 17