Yohane 13:24-26 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

24. Pamenepo Simoni Petro anamkodola nanena naye, Utiuze ndiye yani amene anena za iye.

25. Iyeyu potsamira pomwepo, pa cifuwa ca Yesu, anena ndi iye. Ambuye, ndiye yani?

26. Ndipo Yesu anayankha, Ndi iyeyu, amene Ine ndidzamsunsira nthongo ndi kumpatsa, Pamenepo, m'mene anasunsa nthongo anaitenga naipatsa Yudase mwana wa Simoni Isikariote.

Yohane 13