Yohane 13:11-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. Pakuti anadziwa amene adzampereka iye; cifukwa ca ici anati, Simuli oyera nonse.

12. Pamenepo, atatha iye kusambitsa mapazi ao, ndi kutenga malaya ace, anaseamanso, nati kwa iwo, Nanga cimene ndakucitirani inu; mucizindikira kodi?

13. Inu mundicha Ine Mphunzitsi, ndi Ambuye: ndipo munena bwino; pakuti ndine amene.

Yohane 13