33. Koma ananena ici ndi kuzindikiritsa imfa yanji akuti adzafa nayo.
34. Pamenepo khamulo linayankha iye, Tidamva ife m'cilamulo kuti Kristu akhala ku nthawi yonse; ndipo Inu munena bwanji, kuti Mwana wa munthu ayenera kukwezedwa? Mwana wa munthu amene ndani?
35. Pamenepo Yesu anati kwa iwo, Katsala kanthawi kakang'ono ndipo kuunika kuli mwa inu. 1 Yendani pokhala muli nako kuunika, kuti mdima sungakupezeni; ndipo woyenda mumdima sadziwa kumene amukako,
36. 2 Pokhala muli nako kuunika, khulupirirani kuunikako, kuti mukakhale ana a kuunikako.Izi Yesu analankhula, nacoka nawabisalira.