Yohane 12:13-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

13. anatenga makwata a kanjedza, naturuka kukakomana ndi iye, napfuula, Hosana; wolemekezeka iye wakudza m'dzina la Ambuye, ndiye Mfumu ya Israyeli.

14. Koma Yesu, m'mene adapeza kaburu anakhala pamenepo; monga mulembedwa:

15. Usaope, mwana wamkazi wa Ziyoni; taona Mfumu yako idza wokhala pa mwana wa buru.

Yohane 12