Yohane 11:24-26 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

24. Marita ananena ndi iye, Ndidziwa kuti adzauka m'kuuka tsiku lomariza.

25. Yesu anati kwa iye, Ine ndine kuuka ndi moyo; wokhulupirira Ine, angakhale amwalira, adzakhala ndi moyo;

26. ndipo yense wakukhala ndi moyo, nakhulupirira Ine, sadzamwalira nthawi yonse. Kodi ukhulupirira ici?

Yohane 11