Yobu 41:16-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

16. Alumikizana lina ndi linzace,Mphepo yosalowa pakati pao.

17. Amamatirana lina ndi linzace,Agwirana osagawanikana.

18. Pakuyetsemula ing'anipitsa kuunika,Ndi maso ace akunga zikope za m'mawa.

19. M'kamwa mwace muturuka miuni,Mbaliwali za moto zibukamo.

20. M'mphuno mwace muturuka utsi,Ngati nkhali yobwadamuka ndi moto wa zinyatsi.

21. Mpweya wace uyatsa makara,Ndi m'kamwa mwace muturuka lawi la moto.

Yobu 41