9. Muja ndinayesa mtambo cobvala cace,Ndi mdima wa bii nsaru yace yakulunga,
10. Ndi kuilembera malire anga,Ndi kuika mipikizo ndi zitseko,
11. Ndi kuti, Ufike mpaka apa, osapitirirapo;Apa adzaletseka mafunde ako odzikuza?
12. Kodi walamulira m'mawa ciyambire masiku ako,Ndi kudziwitsa mbanda kuca malo ace;
13. Kuti agwire malekezero a dziko lapansi,Nakutumule oipa acokeko?
14. Lisandulika ngati dothi lonyata pansi pa cosindikiza,Ndi zonse zibuka ngati cobvala;
15. Ndi kuunika kwa oipa kuletsedwa kuti asakuone,Ndi dzanja losamulidwa lityoledwa.
16. Kodi unalowa magwero a nyanja?Kodi unayendayenda pozama peni peni?
17. Kodi zipata za imfa zinabvumbulukira iwe?Kapena kodi unaona zipata za mthunzi wa imfa?
18. Kodi unazindikira citando ca dziko lapansi?Fotokozera, ngati ucidziwa conse.