Yobu 38:2-6 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. Ndani uyu adetsa uphungu,Ndi mau opanda nzeru?

3. Udzimangire m'cuuno tsono ngati mwamuna;Ndikufunsa, undidziwitse.

4. Unali kuti muja ndinaika maziko a dziko lapansi?Fotokoza ngati udziwa kuzindikira.

5. Analemba malire ace ndani, papeza udziwa?Anayesapo cingwe cace ndani?

6. Maziko ace anakumbidwa pa ciani?Kapena anaika ndani mwala wace wa pangondya,

Yobu 38