Yobu 38:10-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Ndi kuilembera malire anga,Ndi kuika mipikizo ndi zitseko,

11. Ndi kuti, Ufike mpaka apa, osapitirirapo;Apa adzaletseka mafunde ako odzikuza?

12. Kodi walamulira m'mawa ciyambire masiku ako,Ndi kudziwitsa mbanda kuca malo ace;

13. Kuti agwire malekezero a dziko lapansi,Nakutumule oipa acokeko?

14. Lisandulika ngati dothi lonyata pansi pa cosindikiza,Ndi zonse zibuka ngati cobvala;

15. Ndi kuunika kwa oipa kuletsedwa kuti asakuone,Ndi dzanja losamulidwa lityoledwa.

16. Kodi unalowa magwero a nyanja?Kodi unayendayenda pozama peni peni?

17. Kodi zipata za imfa zinabvumbulukira iwe?Kapena kodi unaona zipata za mthunzi wa imfa?

Yobu 38