21. Ndipo tsopano anthu sakhoza kupenyerera kuunika pakunyezimira kuthambo,Ndi mphepo yapita ndi kuuyeretsa,
22. Kucokera kumpoto kudzera kuwala konyezimira,Mulungu ali nao ukulu woopsa.
23. Kunena za Wamphamvuyonse, sitingamsanthule; ndiye wa mphamvu yoposa;Koma mwa ciweruzo ndi cilungamo cocuruka samasautsa.
24. M'mwemo anthu amuopa,Iye sasamalira ali yense wanzeru mumtima.