17. Kodi mudziwa umo zobvala zanu zifundira,Pamene dziko liri thuu cifukwa ca mwela?
18. Kodi muyala thambo pamodzi ndi Iye,Ndilo lolimba ngati kalirole woyengeka?
19. Mutilangize cimene tidzanena ndi Iye;Sitidziwa kulongosola mau athu cifukwa ca mdima.
20. Kodi munthu ayenera kumuuza kuti ndifuna kunena,Kapena kodi munthu adzakhumba kumezedwa?