27. Popeza anapambuka, naleka kumtsata,Osasamalira njira zace ziri zonse.
28. M'mwemo anafikitsa kwa Iye kupfuula kwa osauka;Ndipo anamva Iye kupfuula kwa ozunzika.
29. Iye akapatsa mpumulo adzamtsutsa ndani?Akabisa nkhope yace adzampenyerera ndani?Cikacitika pa mtundu wa anthu, kapena pa munthu, ncimodzimodzi;
30. Kuti munthu wonyoza Mulungu asacite ufumu,Ndi anthu asakodwe mumsampha,
31. Pakuti pali wina kodi anati kwa Mulungu,Ndasenza kulanga kwanu, ndingakhale sindinalakwa?