1. Komatu, Yobu, mumvere maneno anga,Mucherere khutu mau anga.
2. Taonani tsono, ndatsegula pakamwa panga,Lilime langa lanena m'kamwa mwanga.
3. Maneno anga aulula ciongoko ca mtima wanga,Ndi monga umo idziwira milomo yanga idzanena zoona.
4. Mzimu wa Mulungu unandilenga,Ndi mpweya wa Wamphamvuyonse umandipatsa moyo.