3. Adapsa mtima pa mabwenzi ace atatu omwe, pakuti anasowa pomyankha; koma anamtsutsa Yobu kuti ali woipa.
4. Ndipo Elihu analindira kulankhula ndi Yobu, popeza akulu misinkhu ndi iwowa.
5. Koma pakuona Elihu kuti anthu atatuwa anasowa poyankha pakamwa pao anapsa mtima.
6. Ndipo Elihu mwana wa Barakeli wa ku Buzi anayankha, nati,Ine ndine mnyamata, inu ndinu okalamba;Cifukwa cace ndinadziletsa, ndi kuopa kukuonetsani monga umo ndayesera ine.