Yobu 31:28-35 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

28. Icinso ndi mphulupulu yoyenera oweruza kunena mlandu wace;Pakuti ndikadakana Mulungu ali m'mwamba.

29. Ngati ndakondwera nalo tsoka la wondida,Kapena kudzitukula pompeza coipa;

30. Ndithu sindinalola m'kamwa mwanga mucimwe,Kupempha motemberera moyo wace.

31. Ngati amuna a m'hema mwanga sanati,Ndani adzapeza munthu wosakhuta nyama yomgawira Yobu?

32. Mlendo sakagona pakhwalala,Koma ndinatsegulira wam'njira pakhomo panga.

33. Ngati ndakwirira zolakwa zanga monga Adamu,Ndi kubisa mphulupulu yanga m'cifuwa mwanga;

34. Popeza ndinaopa unyinji waukuru,Ndi cipepulo ca mapfuko cinandiopsetsa;Potero ndinakhala cete osaturuka pakhomo panga.

35. Ha! ndikadakhala naye wina wakundimvera,Cizindikilo canga sici, Wamphamvuyonse andiyankhe;Mwenzi ntakhala nao mau akundineneza analemberawo mdani wangal

Yobu 31