Yobu 30:27-30 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

27. M'kati mwanga mupweteka mosapuma,Masiku a mazunzo andidzera.

28. Ndiyenda ndiri wothimbirira osati ndi dzuwa ai;Ndinyamuka mumsonkhano ndi kupfuula,

29. Ndiri mbale wao wa ankhandwe,Ndi mnansi wao wa nthiwatiwa.

30. Khungu langa lada, nilindipfundukira;Ndi mafupa anga awawa ndi kutentha kwao.

Yobu 30