14. Akudza ngati opitira pogamuka linga papakuru,Pakati pa zopasuka adzigubuduza kundidzera ine.
15. Anditembenuzira zondiopsa,Auluza ulemu wanga ngati mphepo;Ndi zosungika zanga zapita ngati mtambo.
16. Ndipo tsopano moyo wanga udzitsanulira m'kati mwanga;Masiku akuzunza andigwira.
17. Nyengo ya usiku mafupa anga awaza mwa ine,Ndi zowawa zondikungudza sizipuma.
18. Mwa mphamvu yaikuru ya nthenda yanga cobvala canga cinasandulika,Cindithina ngati pakhosi pa maraya anga.