7. Muja ndinaturuka kumka kucipata kumudzi,Muja ndinakonza pokhala panga kukhwalala,
8. Anyamata anandiona nabisala,Okalamba anandinyamukira, nakhala ciriri,
9. Akalonga anadziletsa kulankhula,Ndi kugwira pakamwa pao;
10. Mau a omveka anali zi,Ndi lilime lao linamamatira ku malakalaka ao.
11. Pakuti pondimva ine khutu, linandidalitsa;Ndipo pondiona diso, linandicitira umboni.
12. Pakuti ndinapulumutsa wozunzika wakupfuula;Mwana wamasiye yemwe wosowa mthandizi.