Yobu 29:21-24 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

21. Anthu anandimvera, nalindira,Nakhala cete, kuti ndiwapangire.

22. Nditanena mau anga sanalankhulanso,Ndi kunena kwanga kunawakhera.

23. Anandilindira ngati kulindira mvula,Nayasama pakamwa pao ngati kulira mvula ya masika.

24. Ndinawaseka akapanda kulimbika mtima;Ndipo sanagwetsa kusangalala kwa nkhope yanga.

Yobu 29