1. Ndipo Yobu anaonjezanso mwambi wace, nati,
2. Ha! ndikadakhala monga m'miyezi yapitayi,Monga m'masiku akundisunga Mulungu;
3. Muja nyali yace inawala pamutu panga,Ndipo ndi kuunika kwace ndinayenda mumdima;
4. Monga umo ndinakhala m'masiku anga olimba,Muja uphungu wa Mulungu unakhala pahema panga;
5. Muja Wamphamvuyonse akali nane pamodzi,Ndi ana anga anandizinga;
6. Muja popondera ine padakhatamira ndi mafuta amkaka,Ndi thanthwe linanditsanulira mitsinje ya mafuta aazitona!
7. Muja ndinaturuka kumka kucipata kumudzi,Muja ndinakonza pokhala panga kukhwalala,