7. Ayala kumpoto popanda kanthu, Nalenjeka dziko pacabe.
8. Amanga madzi m'mitambo yace yocindikira;Ndi mtambo sung'ambika pansi pace,
9. Acingira pa mpando wace wacifumu,Nayalapo mtambo wace.
10. Analembera madziwo malire,Mpaka polekeza kuunika ndi mdima.
11. Mizati ya thambo injenjemera,Ndi kudabwa pa kudzudzula kwace.