14. Kukaca auka wambanda, napha wosauka ndi waumphawi;Ndi usiku asanduka mbala.
15. Ndipo diso la wacigololo liyombekezera cisisira,Ndi kuti, Palibe diso lidzandiona;Nabvala cophimba pankhope pace.
16. Kuli mdima aboola nyumba,Usana adzitsekera,Osadziwa kuunika.
17. Pakuti iwo onse auyesa m'mawa mthunzi wa imfa;Pakuti adziwa zoopsa za mthunzi wa imfa.
18. Atengedwa ngati coyandama pamadzi;Gawo lao litembereredwa padziko;Sadzalunjikanso njira ya minda yamphesa.
19. Cirala ndi dzuwa zitha madzi a cipale cofewa,Momwemo manda acita nao ocimwa.
20. M'mimba mudzamuiwala; mphutsi zidzamudya mokondwera.Sadzamkumbukilanso;Ndipo cosalungama cidzatyoledwa ngati mtengo.