17. Amene anati kwa Mulungu, Ticokereni;Ndipo, Angaticitire ciani Wamphamvuyonse?
18. Angakhale Iye adadzaza nyumba zao ndi zabwino;Koma uphungu wa oipa unditalikira.
19. Olungama aciona nakondwera; Ndi osalakwa awaseka pwepwete,
20. Ndi kuti, Zoonadi, otiukirawo alikhidwa,Ndi zowatsalira, moto unazipsereza.
21. Uzolowerane ndi Iye, nukhale ndi mtendere;Ukatero zokoma zidzakudzera,
22. Landira tsono cilamulo pakamwa pace,Nuwasunge maneno ace mumtimamwako.