Yobu 21:29-34 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

29. Simunawafunsa kodi opita m'njira?Ndipo simusamalira zotsimikiza zao?

30. Zakuti munthu woipa asungika tsiku la tsoka?Naturutsidwa tsiku la mkwiyo?

31. Adzamfotokozera ndani njira yace pamaso pace?Nadzamlipitsa ndani pa ici anacicita?

32. Potsiriza pace adzapita naye kumanda,Nadzadikira pamanda pace,

33. Zibuma za kucigwa zidzamkomera.Adzakoka anthu onse amtsate,Monga anamtsogolera osawerengeka.

34. Potero munditonthozeranji nazo zopanda pace,Popeza m'mayankho mwanu mutsala mabodza okha?

Yobu 21