5. Kuti kupfuula kokondwera kwa woipa sikukhalira kutha,Ndi cimwemwe ca wonyoza Mulungu cikhala kamphindi?
6. Cinkana ukulu wace ukwera kumka kuthambo,Nugunda pamitambo mutu wace;
7. Koma adzatayika kosatha ngati zonyansa zace;Iwo amene adamuona adzati, Ali kuti iye?
8. Adzauluka ngati loto, osapezekanso;Nadzaingidwa ngati masomphenya a usiku.
9. Diso lidamuonalo silidzamuonanso;Ndi malo ace sadzampenyanso.
10. Ana ace adzapempha aumphawi awakomere mtima;Ndi manja ace adzabweza cuma cace.
11. Mafupa ace adzala nao unyamata wace,Koma udzagona naye pansi m'pfumbi.
12. Cinkana coipa cizuna m'kamwa mwace,Cinkana acibisa pansi pa lilime lace;
13. Cinkana acisunga, osacileka,Naoikhalitsa m'kamwa mwace;