Yobu 20:17-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

17. Sadzapenyerera timitsinje,Toyenda nao uci ndi mafuta.

18. Cimene adagwiriraco nchito, adzacibweza, osacimeza;Sadzakondwera monga mwa zolemera zace adaziona.

19. Pakuti anapsinja, nasiya aumphawi;Analanda nyumba mwaciwawa, imene sanaimanga.

20. Popeza sanadziwa kupumula m'kati mwace,Sadzalanditsa kanthu ka zofunika zace.

Yobu 20