Yobu 19:3-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. Kakumi aka mwandicititsa manyazi;Mulibe manyazi kuti mundiumira mtima.

4. Ndipo ngati ndalakwa ndithu,Kulakwa kwanga kuli ndi ine ndekha.

5. Ngati inu mudzikuza ndithu pa ine,Ndi kundichulira mtonzo wanga kuti munditsutse nao;

6. Dziwani tsopano kuti Mulungu wandikhotetsera mlandu wanga,Nandizinga ndi ukonde wace.

7. Taonani, ndipfuula kuti, Ciwawa! koma sandimvera;Ndikuwa, koma palibe ciweruzo.

8. Iye ananditsekera njira kuti ndisapitireko,Naika mdima poyendapo ine.

Yobu 19