Yobu 18:17-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

17. Cikumbukilo cace cidzatayika m'dziko,Ndipo adzasowa dzina kukhwalala.

18. Adzamkankha acoke ku kuunika alowe kumdima;Adzampitikitsa acoke m'dziko lokhalamo anthu.

19. Sadzakhala naye mwana kapena cidzukulu mwa anthu amtundu wace,Kapena wina wotsalira kumene anakhalako.

20. Akudza m'mbuyo adzadabwa nalo tsiku lace,Monga aja omtsogolera anagwidwa mantha.

21. Zoonadi, zokhalamo osalungama zitero,Ndi malo a iye amene sadziwa Mulungu ndi awa.

Yobu 18