8. Anthu oongoka mtima adzadabwa naco,Ndi munthu wosalakwa adzadziutsa kumtsotsa wonyoza Mulunguyo.
9. Koma wolungama asungitsa njira yace,Ndi iye wa manja oyera adzakulabe mumphamvu.
10. Koma bwerani inu nonse, idzani tsono;Pakuti sindipeza mwa inu wanzeru.
11. Masiku anga apitirira, zolingirira zanga zaduka,Zace zace zomwe za mtima wanga.
12. Zisanduliza usiku ukhale usana;Kuunika kuyandikana ndi mdima.