8. Kundigwira kwanu, ndiko umboni wonditsutsa,Kuonda kwanga kundiukira, kucita umboni pamaso panga.
9. Iye ananding'amba m'kundida kwace, nakwiya nane,Anandikukutira mano;Mdani wanga ananditong'olera maso ace.
10. Iwo anandiyasamira pakamwa pao;Anandiomba pama ndi kunditonza;Asonkhana pamodzi kunditsutsa.
11. Mulungu andipereka kwa osalungama,Nandiponya m'manja a oipa.
12. Ndinali mkupuma, koma anandityola;Inde anandigwira pakhosi, nandiphwanya;Anandiimika ndikhale candamali.
13. Eni mauta ace andizinga,Ang'amba imso zanga, osazileka;Natsanulira pansi ndulu yanga.
14. Andipasula-pasula;Andithamangira ngati wamphamvu.
15. Ndadzisokerera ciguduli ku khungu langa,Ndipo ndaipsa mphamvu yanga m'pfumbi.
16. Nkhope yanga njodetsedwa ndi kulira misozi,Ndi pa zikope zanga pali mthunzi wa imfa;
17. Pangakhale palibe ciwawa m'manja mwanga,Ndi pemphero langa ndi loyera.
18. Dziko iwe, usakwirire mwazi wanga,Ndi kulira kwanga kusowe popumira.
19. Tsopanonso, taona, mboni yanga iri kumwamba,Ndi nkhoswe yanga ikhala m'mwamba.