Yobu 15:33-35 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

33. Adzayoyoka zipatso zace zosapsa ngati mpesa,Nadzathothoka maluwa ace ngati mtengo wazitona.

34. Pakuti msonkhano wa onyoza Mulungu udzakhala cumba,Ndi moto udzapsereza mahema a olandira cokometsera mlandu.

35. Aima ndi cobvuta, nabala mphulupulu,Ndi m'mimba mwao mukonzeratu cinyengo.

Yobu 15