Yobu 15:11-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. Masangalatso a Mulungu akucepera kodi?Kapena uli naco cinsinsi kodi?

12. Mtima wako usonthokeranji nawe?Maso ako aphethira-phethira cifukwa ninji?

13. Kuti utembenuza mzimu wako utsutsane ndi Mulungu,Ndi kulola mau otere aturuke m'kamwa mwako.

14. Munthu nciani kuti akhale woyera,Wobadwa ndi mkazi kuti akhale wolungama?

15. Taona, Mulungu sakhulupirira opatulika ace;Ngakhale m'mwamba simuyera pamaso pace,

16. Koposa kotani nanga munthu wonyansa ndi wodetsa,Wakumwa cosalungama ngati madzi.

17. Ndidzakuonetsa, undimvere;Cimene ndinaciona, ndidzakufotokozera;

18. Cimene adacinena anzeru,Adacilandira kwa makolo ao, osacibisa;

Yobu 15