Yobu 13:23-26 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

23. Mphulupulu zanga ndi zocimwa zanga ndi zingati?Mundidziwitse kulakwa kwanga ndi cimo langa,

24. Mubisiranji nkhope yanu,Ndi kundiyesa mdani wanu?

25. Kodi mudzaopsa tsamba lakungouluka,Ndi kulondola ziputu zouma?

26. Pakuti mundilembera zinthu zowawa,Ndi kundipatsa ngati colowa mphulupulu za ubwana wanga.

Yobu 13