18. Taonani tsono, ndalongosola mlandu wanga;Ndidziwa kuti adzandimasula ndiri wolungama,
19. Ndaniyo adzatsutsana nane?Ndikakhala cete, ndidzapereka mzimu wanga.
20. Zinthu ziwiri zokha musandicitire,Pamenepo sindidzabisalira nkhope yanu:
21. Mundicotsere dzanja lanu kutali,Ndi kuopsa kwanu kusandicititse mantha.