Yobu 12:3-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. Koma inenso ndiri nayo nzeru monga inu.Sindingakucepereni;Ndani sadziwa zonga izi?

4. Ndine ngati munthu wosekedwa ndi mnansi wace,Ndinaitana kwa Mulungu, ndipo anandiyankha;Munthu wolungama wangwiro asekedwa.

5. Munthu wosatekeseka apeputsa tsoka mumtima mwace,Limlindira woterereka mapazi ace.

6. Mahema a acifwamba akhala mumtendere,Ndi iwo oputa Mulungu alimbika mtima:Amene Mulungu amadzazira dzanja lao.

7. Tafunsira tsono kwa nyamazo, zidzakulangiza,Ndi mbalame za m'mlengalenga, zidzakuuza;

8. Kapena ulankhule ndi dziko lapansi, lidzakulangiza;Ndi nsomba za kunyanja, zidzakufotokozera,

Yobu 12