Yobu 11:11-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. Pakuti adziwa anthu opanda pace,Napenyanso mphulupulu, ngakhale saisamalira.

12. Koma munthu wopanda pace asowa nzeru,Ngakhale munthu abadwa ngati mwana wa mbidzi.

13. Ukakonzeratu mtima wako,Ndi kumtambasulira Iye manja ako;

14. Mukakhala mphulupulu m'dzanja lako, uicotseretu kutali,Ndi cisalungamo cisakhale m'mahema mwako;

Yobu 11