11. Cifukwa cace Yehova adzamkwezera Rezini olimbana naye, nautsa adani ace;
12. Aramu patsogolo ndi Afilisti pambuyo; ndipo iwo adzadya Israyeli ndi kukamwa koyasama. Mwa izi zonse mkwiyo wace sunacoke, koma dzanja lace liri citambasulire.
13. Koma anthu sanatembenukire kwa Iye amene anawamenya, ngakhale kufuna Yehova wa makamu.
14. Cifukwa cace Yehova adzadula mutu wa Israyeli ndi mcira wace; nthambi ya kanjedza ndi mlulu, tsiku limodzi.