13. Monga munthu amene amace amtonthoza mtima, momwemo ndidzatonthoza mtima wanu; ndipo mudzatonthozedwa mtima m'Yerusalemu.
14. Ndipo mudzaciona, ndipo mtima wanu udzasangalala, ndipo mafupa anu adzakula ngati msipu; ndipo dzanja la Yehova lidzadziwika ndi atumiki ace, ndipo adzakwiyira adani ace.
15. Pakuti taonani, Yehova adzafika m'moto, ndi magareta ace adzafanana ndi kabvumvulu; kubwezera mkwiyo wace ndi ukali, ndi kudzudzula ndi malawi amoto,
16. Pakuti Yehova adzatsutsana ndi moto, ndi lupanga lace, ndi anthu onse; ndi ophedwa a Yehova adzakhala ambiri.
17. Iwo amene adzipatulitsa nadziyeretsa, kuti amuke kuminda tsatane tsatane, ndi kudya nyama ya nkhumba, ndi conyansa, ndi mbewa, adzathedwa pamodzi, ati Yehova.