Yesaya 65:1-3 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Iwo amene sanafunsa za Ine andifunafuna; ndi iwo amene sanandipwaira andipeza; ndinati, Taonani Ine, taonani Ine, kwa mtundu umene sunachula dzina langa.

2. Ndatambasulira manja anga tsiku lonse kwa anthu opanduka, amene ayenda m'njira mosati mwabwino, kutsata maganizo ao ao;

3. anthu amene andiputa Ine kumaso kwanga nthawi zonse, apereka nsembe m'minda, nafukizira zonunkhira panjerwa;

Yesaya 65